spot_img
Tuesday, December 24, 2024
spot_img
HomeLatestGood Samaritan Abida Mia hands over under five-clinic in her Constituency 

Good Samaritan Abida Mia hands over under five-clinic in her Constituency 

Pofuna kulimbikitsa ntchito za uchembere wabwino komanso umoyo wabwino kwa amayi ndi ana aang’ono kumadera a kumidzi, Phungu wa dera la Chikwawa Nkombezi a Abida Mia watsegulira ndi kupereka chipatala cha ‘Under 5’ kwa anthu a m’midzi ya pansi pa Group Village headman Saopa.

A Mia, omwenso ndi Nduna yoona za chisamaliro cha madzi komanso ukhondo ati akuyesetsa kuti amayi asamayende ulendo wautali posaka thandizo la chipatala.

“Tikulimbikitsa kuti amayi apeze chisamaliro choyenera komanso munthawi yake, zimene zilimbikitse uchembere wabwino, komanso kuthandiza kupulumutsa miyoyo,” atero a Mia.

Chipatalachi chamangidwa ndi ndalama za m’thumba la ndalama za CDF zokwana pafupifupi K28 million.-(Times)

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular