spot_img
Friday, December 27, 2024
spot_img
HomeLatestChakwera akwera ndege yaulele

Chakwera akwera ndege yaulele

Kutsatira kuyitanidwa kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus McCarthy Chakwera kuti akakhale mlendo wolemekezeka pa chionetsero chazamalonda chachitatu cha China-Africa Economic and Trade Expo (CAETE), dziko la Peoples Republic of China sabata ino litumiza ndege yokwana anthu 300 makamaka kwa mtsogoleri wa dziko lino komanso nthumwi zake.

Pomvetsetsa bwino za mavuto azachuma omwe dziko la Malawi likukumana nawo pakali pano, dziko la China lalonjeza kukalipira chilichonse chomwe chikafunike panthawi yomwe mtsogoleri wadziko lino komanso nthumwi zake zikakhale zili m’dziko la China.

Uthenga ochokera ku Capital Hill wati zomwe dziko la China lachitazi zipindulira kwambiri dziko la Malawi chifukwa mipando ina mundegeyi ikhala ya amalonda aku Malawi omwe akuyenera kupindula nawo pachiwonetsero cha zamalondachi.

Nthumwi zina zam’mayiko amu Africa zochokera ku Tanzania ndi Kenya zapempha dziko la Malawi kuti liwaganizire zowatenga kupita nawo kuchionetserochi ngati malo angapezeke mundegeyi pomwe a Chakwera akhale akunyamuka kupita ku China.

Chiwonetsero chachitatu cha China-Africa Economic and Trade Expo chidzachitika kuyambira pa 29 June mpaka 2 July 2023 ku Changsha, Province la Hunan, China.

Chionetsero chazamalondachi chizachitika pa mutu woti “Common Development for Shared Future,” ndipo chikuthandizidwa ndi Unduna wa Zamalonda wa People’s Republic of China (MOFCOM) ndi People’s Government of Hunan Province.

RELATED ARTICLES

1 COMMENT

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular