Pa chichewa pali mwambi woti ‘mwamuna nzako akavula kumayamikira, inde kuyamika kuti mzanga uli ndi chi m’dalitso’, Mphunzitsi wakale watimu yampira wamiyendo ya dziko lino Ma rian Mario Marinica wayamikira Patrick Mabedi kamba kochita chamuna kumpikisano wa Cosafa wachaka chino omwe ukuchitikira ku Durban dziko la South Africa.
Timu ya Malawi yalephera kufika ndime yotsiriza ya mpikisanowu itagonjesedwa ndi timu ya Lesotho Lachisanu; pomwe yafa ndi zigoli 3 kwa duuu kudzera pa mapenalty mumphindi 90 masewero atathera 1-1.
Kuti ifike apa, timuyi inapambana masewero ake amagulu omwe anali nawo potsatira kugonjetsa Comoros, Seychelles komanso Zambia.
Osewera a timu ya Malawi anagwiritsa mapenalty atatu pomwe Anyamata a Lesotho anagoletsa mapenalty atatu onse.
Anyamata a Mabedi akhale akusewera ndi South Africa mumasewero ofuna kupeza timu yomwe ithere panambala yachitatu potengera kuti South Africa yagonja dzulo 2-1 nditimu ya Zambia.
“Ndiyamikire Mabedi komanso anyamata pantchito yotamandika yomwe agwira kumpikisano wachaka chino, Palibe yemwe amapereka mpata kuti angachite motere.
“Mabedi ndimphunzitsi odziwa pantchito yache ndiye chifukwa munthawi yomwe ndinali mphunzitsi wa Malawi ndinamukhulupilira kuti akhale wachiwiri wanga,” watero Marinica kuuza Garry Chirwa wa Nation Newspaper.