spot_img
Friday, December 27, 2024
spot_img
HomeLatestBambo ofuna kugwirilira mayi ake amuchepesela chilango

Bambo ofuna kugwirilira mayi ake amuchepesela chilango

Bwalo lamilandu ku Lilongwe lachotsera zaka 8 pa chigamulo cha zaka 14 chomwe a Bester Nyirenda adalandira pa mlandu womwe adapalamula m’chaka cha 2020.

Bambo Nyirenda anagamulidwa ndi bwalo la First Grade Magistrate m’boma la Kasungu kuti alandire chilango atapezeka olakwa pa mlandu wofuna kugwirilira mayi awo.

Pa nthawi yomwe anapezeka olakwa kubwalo laling’onoli, a Nyirenda ankakhala nyumba imodzi ndi mayi awo ndipo usiku wina adalowa kuchipinda kwa mayiwo.

Atalowa, adayesa kuti agone ndi mayi awo ndipo mayiwo atazindikila zomwe zimachitika, adakuwa ndikuchititsa kuti mwana wawoyu aleke nsanga ndikutuluka kuchipindako atapepesa.

Apolisi atawamanga a Bester Nyirenda, adapita nawo kubwalo lamilandu komwe adavomera mlanduwu.

Bwaloli lidatsimikizanso kuti zomwe ankachita kuchipinda kwa mayi wawo zidali zofunitsitsa kuti agone nawo.

Pomwe mlanduwu udabwerelanso kubwalo lamilandu lalikulu kuti chigamulo achiunikire, Nyirenda amaimiliridwa ndi Legal Aid Bureau.

Pounikanso chigamulochi, Justice Bruno Kalemba wati kunalidi koyenera kunjata bamboyu.

Komabe, malingana ndi bwalo lalikululi, chilango chake chimayenera kukhala chofewerapo chifukwa adavomera kulakwa kwake, kadali koyamba kupalamula, sadavulaze aliyense, komanso adapepesa.

Bwaloli kotero latsimikiza kuti m’malo mokhala kundende zaka 14, iwowa agwire chilango chawo kwa zaka zisanu ndi chimodzi (6).

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular