spot_img
Thursday, December 26, 2024
spot_img
HomeLatestMACRA ikutilanga pa tchimo loti si lanthu, Yatero MultiChoice Malawi

MACRA ikutilanga pa tchimo loti si lanthu, Yatero MultiChoice Malawi

Kampani ya Multichoice Malawi yati bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority – MACRA likuwalipiritsa pa tchimo lomwe iwo sadachite.

Malingana ndi chikalata chomwe wasainira ndi m’modzi mwa akuluakulu a kampaniyi Zena Malunje, ntchito za DSTV sizimawakhudza ponena kuti iwo amapereka ntchito za GOtv zokha.

Izi zikutsatira chikalata cha posachedwapa cha MACRA chomwe chati Multichoice Malawi ipereke ndalama za msonkho zokwana K19 million pasanathe masiku makumi atatu – 30 potsatira kuimitsa ntchito za DSTV ndi kampani ya Multichoice Africa Holdings.

Multichoice Malawi yati ipitilira kukambiranabe ndi MACRA kufuna kuyenda limodzi chitsogolo.-(Credit: Capital FM)

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular