spot_img
Wednesday, January 15, 2025
spot_img
HomeLatestMalawi ikuchita bwino pa mayeso a IMF

Malawi ikuchita bwino pa mayeso a IMF

Dziko la Malawi lapambana mayeso oyamba a International Monetary Fund (IMF) pomwe bungwe loona za chuma padziko lonse lapansi lafika pa mgwirizano ndi boma pa mmene chuma chingayendele popita chitsogolo.

Izi zitsimikizika akuluakulu oyendetsa bungwe la IMF akakumana ndi kuvomeleza mgwilizano wu.

Potengera izi, Dziko la Malawi likhala ndi mwayi opatsidwa ngongole ya ndalama zokwana pafupifupi K195 biliyoni pansi pa ndondomekoyi maaka akuluakulu oyendetsa IMF akavomereza izi.

Nduna ya zachuma a Sosten Gwengwe yati Mabwana aku IMF akakavomereza ndalama zapafupifupi K195 billion zandondomeko ya ECF zichititsa kuti abwenzi adziko lino monga World Bank komanso European Union ayambe kubweretsa ndalama zothandizira ndondomeko yachuma cha dziko lino.

Izi zili chomwechi ati kaamba koti mabungwe onsewa amadikilira bungwe la IMF kuti liyamikire zomwe bungweli linagwilizana ndi Boma la Malawi ndipo poti gawo loyambali latheka thandizo la chuma lomwe lingabwere ndi maiko ena lithandiza kuti ntchito zachuma cha dziko lino zomwe zinasokonekera kaamba ka Namondwe Anna, Gombe, Mliri wa Covid-19 komanso kolera zibwelere mchimake.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular