spot_img
Tuesday, December 24, 2024
spot_img
HomeHealthTSEKETSEKE: Bambo wazaka 70 wamwalira ali mkati 'mothira batire' hule

TSEKETSEKE: Bambo wazaka 70 wamwalira ali mkati ‘mothira batire’ hule

Bambo wazaka 70 zakubadwa  wapezeka atafa kumalo ogona alendo ku Chitakale m’boma la Mulanje, pomwe zadziwikanso kuti anali ndi mkazi wachibwenzi.

Mneneri wapolisi ku Mulanje, Innocent Moses, wati bamboyo, yemwe dzina lake ndi Lemon Walama, amagwira ntchito ngati wachitetezo pamalopo.

Malinga ndi a Moses, malemuwo anapeza mkazi wachibwenzi ndipo analowa naye mchipinda cha pamalopo kuti akasangalale ndipo anamwa mankhwala owonjezera chisangalalo.

Mmawa watsiku lotsatira, bamboyo anapezeka atafa ndipo zotsatira zachipatala zasonyeza kuti bamboyo wamwalira chifukwa cha matenda a mtima,

Matenda wa ati anayamba chifukwa cha kuthamanga kwa magazi kaamba ka mankhwala owonjezera chisangalalo anamwawo. Pakadali pano, mkaziyo ali mmanja mwa apolisi kuti afotokoze zambiri zankhaniyi.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular