spot_img
Saturday, November 23, 2024
spot_img
HomeLatestProphet Phiri wakana mlandu othira 'batire' mwana wake

Prophet Phiri wakana mlandu othira ‘batire’ mwana wake

…. Amandiseweretsa mawere ndi ndata, umboni wa mwana

Bwalo la milandu ku Mangochi layamba kumva mlandu wa mneneri wa mpingo wa Supernatural Embassy ku Mangochi yemwe akumuganizira kuti amachita zachisembwere ndi mwana wake wa zaka 16 za kubadwa.

Mboni yoyamba yaboma pamulanduwu anali mtsikanayu yemwe umboni wake anaumvera mu kachipinda komata.

Mboni ya chiwiri ndi mai ake a mtsikanayu omwe atsimikizira bwalo lamilandu kuti amuna awo akale a Christopher Phiri amagonana naye mtsikana yo.

Atafunsidwa ngati ali ndi umboni omwe ukutsimikiza kuti izi zinachitikadi maiwo akuti anaona zithunzi zosakhala bwino komanso iwowo atamufunsa mwanayo anavomera kuti izi zimachitikadi.

Koma yemwe akuimira a Phiri pa mlanduwu, anauza bwalo kuti zithunzi zomwe maiwo akunena kuti anaonazo sizikutsimikiza kuti bamboyo amagonanadi ndi mwanayo.

Komanso muumboni wake mwanayo mukachipinda komata akuti wayankha kuti sanagonaneko ndi bambo akewo koma kuti amangomuseweretsa mawere ndi malo obisika.

Bwalo lamilandu likupitilira kumva umboni kuchokera kwa ogwira ntchito kuchipatala.Mulanduwu wachititsa chidwi anthu ambiri mderali.

Ena omwe anali pa bwaloli ati amafuna adzadzimvere okha kuti chadza ni yani kuti mtumiki aganiziridwe kuchita chisembwere ndi mwana wake yemwe.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular