spot_img
Monday, December 23, 2024
spot_img
HomeLatestNdizapikisana nawo pa pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko-Nankhumwa

Ndizapikisana nawo pa pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko-Nankhumwa

Yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive-DPP a Kondwani Nankhumwa ati adzapikisana nawo pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chomwe chikuyembekezeka kuchitika chaka cha mawa.

A Nankhumwa, omwe anachotsedwa m’chipani cha DPP kaamba kogawukira komanso kudelera utsogoleri wake, anena izi lero ku Ndirande- Malabada muzinda wa Blantyre.

Malingana ndi a Nankhumwa, akuluakulu a chipani cha DPP anawachotsa m’chipanichi kamba koti anaonetsa chidwi chofuna kudzapikisana nawo pa chisankho cha mtsogoleri wa chipani cha DPP.

A Nankhumwa, omwe akuyembekezereka kuwuza a Malawi za tsogolo lawo pa ndale sabata ino, ati maloto omwe anali nawo odzapikisana nawo pa chisankho cha mtsogoleri sanafe.

Nankhumwa, omwenso ndi phungu wa m’dera la pakati m’boma la Mulanje, anachotsedwa chipanichi pamodzi ndi anthu ena, omwe ndi kuphatikizapo Grezelder Jeffrey, Cecilia Chazama, Nicholas Dausi mwa ena.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular