spot_img
spot_img
10.8 C
New York
Tuesday, November 12, 2024
spot_img
spot_img

Anthu ena akufuna kundiyambanitsa ndi a Chilima, atero a Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati pali kagulu kena ka anthu komwe kakufuna ku wayambanitsa iwo ndi wachiwiri wawo a Saulos Chilima.   

A Chakwera anena izi lero pa msokhano wa chitukuko pa bwalo la za masewera la Chinsapo mu mzinda wa Lilongwe.

M’mawu awo anati anthu ena amakonda kudanitsa komanso kuyambanitsa anthu ndipo ayesera kangapo konse kudanitsa iwo ndi a Chilima koma alephera.

“Ndikuziwa kuti pali anthu ena omwe akufuna kutiyambinitsa ndi a Chilima komanso zina mwa nduna zanga,” anatero a Chakwera

Malingana ndi a Chakwera, iwo sapanga nawo ndale zodanitsa, zotukwana ena komanso zonyoza ena.

Pamenepa a Chakwera anapempha a Malawi komanso a ndale ena kuti asiye ndale zosungirana ka m’peni ku mphasa.  

Iwo ati a nthawi yakwana kuti a Malawi agwirane manja pa ntchito yotukula dziko lino osati kungokhalira ‘ukavundula madzi’.  

Pakhala pali phekesera zoti a Chakwera omwe ndi a chipani cha Malawi Congress (MCP) komanso a chiwiri awo a Chilima a chipani cha UTM akhala asakugwirizana.

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -

Latest Articles