
Mtsogoleri wachipani chotsutsa cha Democratic Progressive Party- (DPP) a Prerofessor Peter Mutharika wasintha thabwa pankhani yoti ayankhula a Malawi komanso President Lazarus Chakwera lero.
Lamulungu lapitali Mutharika, kudzera mmneneri wake bambo Shadrick Namalomba, anati alankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana lero La Chitatu makamaka pa zautsogoleri wa Tonse.
Koma a Namalomba, mneneri wa Mutharika komanso chipani cha DPP, kudzera mu kalata ati mtsogoleri wakale wa dziko lino yu ayankhulabe mtsogolomu.