Bwalo la milandu la Principal Resident Magistrate ku Zomba lagamula kuti a Ganizani Mtaila apatsidwe chipepeso cha K2.8 miliyoni kaamba komangidwa ali osalakwa ndi kukhala kundende masiku 14.
Malinga ndi chikalata chochokera ku nthambi yoimira anthu mwaulere pa milandu ya Legal Aid Bureau, patha zaka 20 kuti a Mtaila alandire chipepesochi.
Zidamveka mβbwalolo kuti mβchaka cha 2003 iwo ankagwira ntchito ya ulonda ku kampani ya Securicor Malawi ndipo tsikulo adali kulondera pa maofesi a kampani ya Fargo ku Limbe mumzinda wa Blantyre.
Mkati mwa usiku adalandira uthenga kuchokera kwa mabwana awo amene amafunsa ngati pa malowo pabedwa koma iwo adakana. Adafunsidwa kangapo, koma iwo adapitiriza kukana.
Apa apolisi adafika pamalowo kudzafufuza koma adapeza kuti padalibe za umbanda.
βKoma mmodzi mwa akapitawo awo adati limodzi ndi anzawo, a Mtaila amangidwe basi. Tsiku lachinayi atamangidwa, adalandira kalata yowaimika pa ntchito ndipo atatuwo adakhala sabata ziwiri mβchitokosi cha polisi ya ku Limbe,β chidatero chikalatacho.
Atapatsidwa belo mlandu wawo udayamba ndipo pakutha kwa miyezi 4 bwalo likumva kuti anayi adathyola nyumba ndi kuba katundu, bwalo lidawapeza osalakwa ndi kunena kuti adalibe mlandu ulionse.
A LAB adautengera mlanduwo kuchoka ku Blantyre kupita ku Zomba chifukwa nβkomwe amakhala.
βNdakondwa kwambiri kuti ndalandira chipepeso ndipo nkhaniyi yatha. Ndakondwa kuti a Legal Aid andithandiza,β adatero a Mtaika.