spot_img
Wednesday, December 25, 2024
spot_img
HomeLatestChiwelengero cha malo oponyera voti chakwera

Chiwelengero cha malo oponyera voti chakwera

Bungwe la Chisankho la MEC, lati chiwelengero cha malo ochitira kalembera wa chisankho chakwera kuchoka pa 5,002 kufika pa 6,344.

Izi malinga ndi mkulu oona zofalitsa nkhani ku bungweli, Sangwani Mwafulirwa ndi kamba ka kuunikilidwanso kwa chiwelengero cha madera a aphungu mdziko muno.

Pa chifukwa ichi, pa chisankho cha chaka cha mawa, kudzakhala mipando 229 ya aphungu kuchoka pa mipando 193, ndi mipando 509 yama khansala kuchoka pa mipando 462.

Pakadali pano, Mwafulirwa wati bungwe lake lilengezabe za chiwelengero cha malo momwe mudzachitikire chisankh.-MIJ ONLINE

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular