By Romeo Umali, MBC Online
Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, walimbikitsa anthu amene ngozi yakusefukira kwa madzi yawakhudza kuti asaganize zodzipha komanso asataye mtima.
A Chakwera ati iwo akambirana ndi a bungwe la NEEF kuti awapatse ngongole anthuwa kuti ayambirenso miyoyo yawo popeza ngozi imeneyi yakhudza anthu ochuluka m’dziko muno.
A Chakwera ati akambilananso ndi a AFDEB kuti akonzenso mlatho wa Dwangwa.
Poyankhula poyambilira, nduna ya maboma ang’ono, a Richard Chimwendo Banda, anati mtsogoleri wa chitsanzo samaonekera nthawi ya mavoti okha koma panthawi ya zovuta.
Iwo anati a Chakwera ndiye bwenzi wa anthu ndipo asasiye mtima okonda, kaamba kakuti adachitanso zimenezi kutachitika ngozi ya namondwe wa Freddy.
Iwo anaonjezeraponso ponena kuti kampani yokonza shuga ya Illovo yagwira ntchito yotamandika popeza ndiyo yathandiza kutsegula malo a Matiki Camp komwe kuli anthu ena okhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi.
Malinga ndi nthambi ya DoDMA, anthu opyola 14000 ndi amene akhudzidwa ndipo anthu asanu ndi awiri ndi amene atisiya.
Nthambiyi posachedwapa ikhala ikubweretsa lipoti latsatanetsatane wa m’mene ngoziyi yaonongera ku Nkhotakota.
Sabata latha masana, kunagwa mvula ya mphamvu yomwe idaoononga malo ambiri m’bomali, maka ku Dwangwa.
M’modzi wa ochita malonda ku Dwangwa, a Alinafe Kachipande, ati ntchito za malonda padakali pano zalowa pansi m’derali kaamba kangozi ya madzi osefukirayi.
M’nawu awo, iwo ati ngoziyi ikanakhala kuti yachitika mkati mwausiku, anthu ambiri akanatisiya.