spot_img
Tuesday, December 17, 2024
spot_img
HomeLatestMWASANDUKA VAN DAMME: Wa Sembe waswa makofi choir master ku Lunzu

MWASANDUKA VAN DAMME: Wa Sembe waswa makofi choir master ku Lunzu

Chi khristu mwachisiya kuti mwasanduka vandame nkhope ngati Rambo Rambo Rambo.

mapemphero asokonekera pa mpingo wa katolika wa Mipande ku Lunzu m’boma la Blantyre wa sembe atamenya otsogolera gulu loimba (choir master) kamba koyambitsa nyimbo ya Aleluya mu nyengo ino ya Rent.

Malinga ndi omenyedwayu, Issac Edward yemweso ndi wapampando wa pa kachisiyu, nthawi yopereka mphatso anayambitsa nyimbo yomwe mkati mwa nyimbomo munadzamveka mau a Aleluya, ndipo nthawi yomweyo akuti wasembe anachoka ku guwa nkupita kukawamenya bakera pakamwa pawo.

Edward wati wasembeyu anawafunsa kuti “mutchula bwanji kuti Aleluya mu nyimbo nyengo ino ya Rent?? Ndipo nthawi yomweyo anadimenya bakera koma sinabwezere” Atero a Edward.

Iwo auza Mij Online kuti wasembeyu atangomaliza kumenya mkuluyo anakakwera galimoto yake nkumapita.

Padakali pano mmodzi mwa akhirisitu omwe analimo mu kachisiyu pa nthawiyi Siza Felix watiuza kuti mapemphero athera panjira ndipo anthu akubalalika.- (Credit: MIJ ONLINE)

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular