spot_img
spot_img
24.7 C
New York
Wednesday, September 11, 2024
spot_img
spot_img

Aphungu akukambirana za chamba

Aphungu a nyumba ya malamulo akukambirana ganizo lokhazikitsa lamulo lomwe lingavomereze ulimi wa chamba chosuta m’dziko muno.

Phungu wadera la kum’mwera kwa boma la Lilongwe, a Peter Dimba, ndiyemwe wabweretsa ganizolo mnyumbayi.

Ena mwa maganizo omwe aphungu apereka pothilira ndemanga ndikuti lamulo lovomereza ulimiwu lidzakhale lokomera alimi achimalawi kuti ambiri adzakhale ndi mwayi opeza phindu lochuluka komanso kupereka mwayi wa ntchito.

Aphunguwa ati, mwazina, ulimi wa chamba utha kuthandiza dziko lino kupeza ndalama zakunja zochuluka.

Ndipo Mtsogoleri wa zokambirana mu nyumbayi, a Richard Chimwendo Banda, ati ulimiwu ndi wabwino koma ndikofunika kuti amalawi aphunzitsidwe zokhudza ulimiwu poopa kubweretsa mavuto pakati pa achinyamata.

Padakali pano, aphunguwa akupitiriza kupereka maganizo awo pa nkhaniyi.-( Credit: MBC Online)

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -

Latest Articles