By Topson Banda, Kasungu Community Radio
Anthu okhudzidwa kwa Nyambo m’dera la mfumu ya ndodo Wimbe m’boma la Kasungu aopsyeza kuti akachita m’bindikiro ku maofesi a bungwe la ESCOM m’bomali.
Izi zikudza pomwe anthuwa akhala opanda magetsi kuchokera m’chaka cha 2021, kutsatira kuonongeka kwa transformer yomwe imkaperekera magetsi m’deralo.
Wapampando wa anthuwa a Byson Mwale wati apereka ma sabata awiri okha ku maofesi a bungweli kuti akawaikire transformer ina kapena awatsimikizire tsiku lenileni lomwe adzalandirenso magetsi.
“Ngati sipachitika chilichonse m’masabata-wa, tikamanga msasa ku maofesi komweko. Zaka zachulukitsa asakutiganizira ndipo takhala tikugogoda ku ESCOM koma ata! Siziphula kanthu.
Chaka chatha a ESCOM anadzachotsa transformer yoonongekayo nkutilonjeza kuti ayika ina sabata yomweyo koma mpaka lero kuli zii! Ma bizinesi anthu anaima kale-kale pano tusowa mntengo wogwira,” atero a Mwale koma mokwiya.
Koma engineer wamkulu ku bungweli m’bomali a Blessing Mwafulirwa watsimikiza kuti alandira chikalata cha madandaulocho.
Komabe a Mwafulirwa ati deralo liri pa mndandanda wa madera omwe alandire ma transformer posachedwapa.