President Lazarus Chakwera lero wadzudzula dziko la Amerika pololowelela pa milandu yokhuza katangale yomwe anthu ena akuyankha ku khoti mdziko muno.
A Chakwera ayankhula izi pomwe amatsekulila mtsonkhano wa zokambilana zofuna kutukula ulimi mdziko muno.
A Chakwera ati dziko la Amerika ndi limodzi mwa maiko omwe anthu ochuluka amaphana ndi mifuti, komanso mchitidwe wa malonda a mankhwala ozunguza bongo uli patsogolo, kuonjezela apo apolisi dzikoli amapha anthu a mtundu wachikuda ochuluka zedi.
A Chakwera ati ku Amerika kuli umbanda wa mnanu moti pa chaka kumakhala milandu yopitilila 10 million ya umbanda.
Choncho, a Chakwera ati ndiodabwa kuti anthu ena amakhala patsogolo kunyozetsa dziko lino pa zofooka zina ndi zina.
Iwo ati mchitidwe omwe a Malawi ena amachita onyozetsa dziko lino, ndi omwe umapangitsa kuti anthu a maiko ena azikhala ndi mphamvu yonyoza dziko lino.
Mau awo, a Chakwera ati makhoti komanso mabungwe ngati ACB ndi oyima paokha ndipo ali ndi ukadaulo ogwila ntchito yayo popanda wina kulowelela.
Sabata lomwe lino dziko la Amerika linatulutsa chikalata chonena kuti anthu anayi , a Reyneck Matemba, George Kainja, John Suzi Banda komanso Mwabi Kaluba ndioletsedwa kulowa mdziko la Amerika chifukwa cha milandu yawo ya katangale.- NATION ONLINE