Mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP), Peter Mutharika walonjedza kukonza dziko lino lomwe akuti lawonongedwa ndi ulamuliro wa Lazarus Chakwera.
A Mutharika, omwenso akuzapikisana nawo pa chisankho cha mchaka cha mawa, anena izi kudzera pa tsamba lawo la mchezo lapa facebook.
Pamenepa, iwo apempha a Malawi kuti agwirane manja maka pokozanso dziko lowonongekali.
Mawu a Mutharika abwera pomwe kwangosala masiku ochepa kuti achititse msonkhano wa ndale mu mzinda wa Blantyre.
Mwa zina, iwo akuyembekezereka kufotokozera a Malawi mfundo zomwe akonza pokozanso dziko la Malawi.