spot_img
Monday, January 6, 2025
spot_img
HomeLatestMlonda amangidwa kaamba kobera Mulungu

Mlonda amangidwa kaamba kobera Mulungu

Apolisi ku Lilongwe amanga bambo wina wa zaka 44 zakubadwa pomuganizira kuti adatchola kachisi wina ndi kubamo zida zoimbira za ndalama zokwana K3.5 million.

Bamboyu akuti amagwira ntchito ngati mlonda pa kachisi wa Time of God mumzinda wa Lilongwe.

Zidazi ndi monga mixer ndi amplifier.

Mneneri wa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu wati bamboyu dzina lake ndi Patrick Zyambo ochokera m’mudzi wa Mzikubola m’dera la mfumu yaikulu Maulabo m’boma la Mzimba.

A Chigalu ati apolisi omwe ankagwira ntchito m’bandakucha wa lachitatu pa 15 May chaka chino adamanga bamboyu atamupeza ndi katunduyu.

“Bamboyu adaulula kuti adaba katunduyu pa kachisichi chimene chiri moyandikana ndi sukulu ya ukachenjede ya Kamuzu University of Health Sciences mu mzindawu. Iye adafotokoza kuti adalowa mkachisiyu ataphwanya zenera lalikulu,” iwo adatero.

Bamboyu akuyembekezereka kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kumene akayankhe mlandu wotchola nyumba ndi kuba.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular