
Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM, Patricia Kaliati wati a Saulos Chilima ndi omwe akuzatsogolera mgwirizano wa Tonse pa chisankho cha chaka cha mawa.
A Kaliati anena izi pa msonkhano wa ndale omwe chipanichi chinali nawo kumapeto kwa sabatayi.
Malingana ndi a Kaliati, UTM ili ndi chikhulupiliro kuti President Lazarus Chakwera ndi munthu wa umunthu komanso ulemu wake ndipo azatsatira mfundo za mgwirizano wa Tonse.

Iwo anasindika kuti a Chilima ndi omwe azayimilire mgwirizano wa Tonse omwe pakadali pano ukutsogozedwa ndi a Chakwera a chipani cha Malawi Congress (MCP).
Malipoti amasonyeza kuti a Chakwera anagwirizana ndi wachiwiri wake kuti ndi yemwe azayimilire mgwirizano wu pa chisankho cha chaka cha mawa.
Ngakhale izi zili chomwechi akuluakulu a zipani ziwirizi akhala akusemphana chichewa pa za mgwirizanowu, pomwe chipani cha MCP chakhala chikutsutsana ndi zomwe a Kaliati akunena.