spot_img
24.1 C
New York
Saturday, June 29, 2024
spot_img
spot_img

Chakwera Ayimanso

Mtsogoleri wa mdziko lino Dr. Lazarus Chakwera wati ndiokonzeka kudzaimira chipani cha Malawi Congress (MCP) pa chisankho cha chaka cha mawa.

Malingana ndi a Chakwera malamulo achipanichi akumulora kukapikisa nao ku chisankho chosankha atsogoleri a chipanichi.

Izi zayankhulidwa pa mnsonkhano wachitukuko omwe unachitikira pabwalo la sukulu ya primary ya Ndaula mu mzinda wa Lilongwe.

A Chakwera ati malamulo achipani cha MCP kuwalora kutsogoleranso chipani chi kwa dzaka zina zisanu ndipo ali okonzeka kuti akapikisane ndi anthu ena ku mnsonkhano waukulu wa chipani chi ndipo akapambana.

Pamenepa, iwo anapitilira kupempha ena kuti akatenge nao gawo popikisana nao mmaudindo osiyanasiyana ku chipani chi.

Iwo apempha anthu mdziko muno kuti akhale osunga lamulo ponena kuti asamatengere malamulo mmanja mwawo.

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -

Latest Articles