Amalawi akuyembekezerabe pamene asilikali ankhondo ndi nthambi zina zaboma akupitilira ndi ntchito yosaka ndege imene inanyamula wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino Dr Saulos Chilima, imene siyidakafike pa ulendo opita ku Mzuzu Airport.
Pali maganizo akuti ndegeyi, imene inanyamula anthu asanu ndi anayi, mwina ili mudera la Chikangawa kumene pakali pano gulu likufunafunabe ndegeyo.
Ndipo boma,kudzera mwa mlembi wamkulu mu ofesi ya prezidenti ndi nduna zake a Colleen Zamba, latsindika kuti likhala likudziwitsa mtundu wa amalawi zimene angapeze amene akugwira ntchito yofunafuna ndegeyi.