spot_img
27.9 C
New York
Friday, July 12, 2024
spot_img
spot_img

Apolisi amanga mayi Matako

Apolisi m’boma la Balaka amanga a Lilian Matako, ochokera mmudzi mwa Kanyumbaka, mfumu yayikulu Sawali m’boma lomwelo powaganizira kuti adamenya mwankhanza mwana wawo wachichepere.

Ofalitsankhani za polisi ya Balaka, a Gladson M’bumpha, wati mayiwa akuganiziridwa kuti adamenya molapitsa mwana wawo Mercy Magombo wa zaka 9, yemwe amaphunzira mu Standade 3 pa sukulu ya Ngwangwa Primary.

Mtsikanayo akuti pa 28 June chaka chino,malinga ndi mayi wakeyo, anaba ndalama yokwana K2000 imene Matako adasiya kunyumba panthawi imene amapita ku geni ndipo atafunsidwa ndikuvomera,mayiyo mothandizidwa ndi anyamata ena anamanga Mercy miyendo ndi manja ndikumumangilira ku mtengo ndipo pamapeto pake adamumenya ndikumuthira madzi osakaniza ndi chitedze.

Malume amwanayo ndiwo adakatsina khutu apolisi lero pa 6 July ndipo mayiyo akuyembekezeka kukaonekera kubwalo lamilandu posachedwapa.

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -

Latest Articles