spot_img
Wednesday, January 15, 2025
spot_img
HomeNationalLazaro wagwera m'chimbudzi

Lazaro wagwera m’chimbudzi

Bambo wina yemwe akuti dzina lake ndi Mavuto Lazaro athamangira naye ku chipatala cha Kasungu, atagwera m’dzenje lomwe akumba kuti chikhale chimbudzi pa mzikiti wa Chitete m’bomali.

Sheikh Amdan Omar wati akuganiza kuti bamboyu anagwera m’dzenjero usiku wapitawu chifuwa anthu amuonamo m’mbanda kucha walero.

A Omar ati atamufunsa, bamboyu anakwanitsa kungotchula dzina lakelo ndi kuti amachokera ku Chiphaso, m’bomali, kotero iwo apempha anthu omwe angadziwe bamboyu kuti akanene ku polisi.

Ena mwa anthu omwe anathandizira kutulutsa bamboyo m’dzenjemo, ati akuganiza kuti bamboyu analedzera.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular