spot_img
Saturday, November 30, 2024
spot_img
HomeLatestUTM itenga boma chaka cha mawa, atero a Kabambe

UTM itenga boma chaka cha mawa, atero a Kabambe

BY Dr. DALITSO KABAMBE

Amayi ndi abambo, atsogoleri komanso nonse otsatira chipani cha UTM, a Malawi anzanga.

Lero, ndine okondwa kwambiri kuti ndikulankhula koyamba ngati membala ovomerezeka wa chipani chotsogola cha UTM.

Otsatira chipanichi konse komwe muli mdziko muno; monga ku Kameme m’boma la Chitipa, kwa Chauma ku Nkhotakota, ku Fatima mboma la Nsanje, ndikwa Kamwendo ku Mchinji, dziwani kuti ndili ndi chimwemwe kuti ndalandilidwa mwa chikondi.

Ngakhale a Dr Chilima, omwe analinso wa chiwiri kwa mtsogoleri wa dziko anatisiya, Malawi sadzakhalanso chimodzimodzi chifukwa mbeu zomwe anadzala, zikhala zikubalabe zipanso mpaka kalekale.

Mbeu monga kudzipereka, kulimbikitsa a Malawi kuti ngakhale nyengo zitalimba bwanji OSAOPA, OSATOPA, OSAFOOKA.

Kotero ndikumemeza a Malawi a kufuna kwabwino omwe amalakalaka atapeza mpumulo wawo pa nkhani za ndale kuti UTM ndiye Khomo lanu. Tiyeni tigwirane manja ndikuthandiza kupititsa patsogolo ntchito yomwe idayambika kaleyi.

UTM si chipani chabe koma ndi mgwirizano okhazikika omwe unabadwa anthu atatutumuka ndi mchitidwe wa tsankho, kunamizana komanso kupusitsana, kukula Kwa umphawi komanso kusalemekeza ufulu wa anthu osiyanasiyana.

Kotero, ganizo lolowa chipani cha UTM, likuchokera pansi pa mtima wanga ndipo ndili ndi chikhulupiliro kuti ndatsata njira yolondora yomwe ndi yokhayo ingaphule dziko la Malawi mu zolemetsa zomwe wakhala akudutsamo.

Pomwe ndale za mdziko muno muli maphokoso ndi chipwiliki, ife tasankha kulunjika kutsogolo ndi cholinga choonetsetsa kuti tsogolo la dziko lino likhale lowala.

Mongochenjezana, ulendowu siophweka; muli minga ndi zisoso, koma tikagwirana manja ndi kudzipereka mwakuya tidzakwanilitsa kumanga dziko lino.

Ndi pemphero langa kuti mu UTM musefukire bata ndi mtendere. Mchipanichi mulitu utsogoleri wa mphamvu omwe umalimbikitsa kulolelana komanso kukambilana ngati pabuka kusamvana.

Izitu ndi zipatso komanso mbeu zomwe anafetsa mtsogoleri wathu malemu a Dr Chilima.

Achinyamata komanso amayi tiyeni tionetsetse kuti tikutsatira utsogoleri okamba mfundo zomanga dziko lino osati nkhambakamwa chabe.

Imani apo pali chilungamo osati maphokoso opanda pache pakuti inu ndiye muli ndi chifungulo cha Malawi otukuka komanso okomera mafuko onse ali nkudza.

Pomwe tikulakalaka kusintha, kudzera mukugwirizana ndi kudzipereka, tiyeni tiuzililire mpweya watsopano mu mmasomphenya athu. Tiyatse nyali zathu za chiyembekezo chifukwa kuthekera kulipo.

Pamodzi, ndili ndi chikhulupiro chozama, kuti tidzatha kugonjetsa. Mdima ungakule bwanji, kumayenera kuche basi.

Ndikudziwa payankhulidwa zambiri m’mene mphekesera zomamveka kuti mwina ndikulowela ku UTM, ndipo ena anali ndi nkhawa pa zolinga zanga.

Ndabwera kukutsimikizilani kuti ngati mene ankanfunila malemu Saulos, tiyeni tikondane ndipo ine ngati DK ndine okonda mtendere ndi bata nthawi zonse.

Chotero, ndikupempha ngati pena ena sanayankhule bwino, tikhululukilane ndikubwera pamodzi ndi cholinga chowombola dziko la Malawi pa ng’anjo ya moto tikudutsamomu.

Ndili ndi chikhulupiliro kuti tikagwirana manja titenga boma chaka cha mawa osakayikilanso.
Ngakhale ndinasankha kutuluka ku DPP mwachete, ndinaona ena akupereka zifukwa zawo zosiyanasiyana pa kuchoka kwanga ku DPP; zifukwa zonyanzitsa, zonyoza, zonyogodola dzina langa.

Ngakhale zili chomwecho, pa umunthu wanga, ndasankha kuwakhululukira, nkuyendabe kumapita chitsogolo chomwe Dzanja la Yehova likunditsogoza.

Ndakhululukiranso ngakhale iwo amakamba za nkhani za dzina langa ku UTM, ndipemphe ku UTM, tiyeni tipitilire kukhala ogwirizana ngati banja limodzi, popewa kugawanitsidwa ndi mabodza a anthu ansanje omwe satifunira zabwino.

Ngakhale nkhani zina zili zowawitsa moyo, zodetseratu dzina langa kotheratu, ndasankhabe kuti nthawi idzavumbulutsa kusalakwa kwanga, ndipo chowonadi chidzakhala pa mbalambanda.

Ino, ndi nthawi yofunikira kwambiri ngati dziko kuti tigwirane manja pothetsa mavuto omwe tili nawo.

Ngati ndale zathu zipitilire kukhala zothana, zatimke nawo, dzikoli silidzasintha, ndipo tidzapitilira kulirira ku utsi. Kulira kwathu, tsono, kudzakhala chisankho chathu.

Koma ndikuwona kuti, ngati dziko, titayima pamodzi, nkugwirana manja ndi UTM, mavuto onse otsamwitsawa tidzagonjetsa ndipo tidzapita patsogolo.

Tichilimike pamgwirizano umenewu, ndikumvetsetsana pamene tikuyenda mchipululu cha mitsamwitso yosiyanasiyana koma tikulimbika pa masomphenya a tsogolo lowala likudza kwa ife tonse tikapambana pa nkhondo imeneyi.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular