spot_img
Tuesday, January 28, 2025
spot_img
HomeLatestMoyo nkudya, moyo ndi nsima, tiyeni tilimbikitse ulimi- Ching'ani

Moyo nkudya, moyo ndi nsima, tiyeni tilimbikitse ulimi- Ching’ani

Emwe akufuna kudzaimira chipani cha Malawi Congress (MCP) pa mpando wa phungu wa kunyumba ya malamulo kudera la kum’mwera kwa boma la Ntcheu, Engineer Joe Ching’ani wayambitsa uli wamakono wa mthilira kudera lakwawo, mfumu yayikulu Tsikulamowa pofuna kuthana ndi njala mderali.

Engineer Ching’ani emwenso ndi wapampando wa Blantyre Water Board wati dera lakumwera kwa boma la Ntcheu ndi lodalitsika kaamba koti lili ndi nthaka yabwino komanso mtsinje wa Lisungwi omwe siuphwa. Komabe iye wati kwakhala kovuta anthu kutukuka ndi izi kaamba kosowa uphungu ndi zipangizo zoyenerera paulimi kuti ukhale wamakono ndi opindula.

Iye amayankhula lachiwiri pomwe amapereka makina atatu opopa madzi ku magulu atatu ochita ulimi omwe ndi Tikondane ndi Nthula a kwa Gulupu Gangawako komanso Tiyanjane ya kwa Gulupu Matchereza onse a pansi pa mfumu yayikulu Tsikulamowa m’boma la Ntcheu. Iye wati akuyembekezeka kuti zipangizozi zichepetsa ntchito yothilira mbeu ndi manja.

“Nthawi zambiri timayang’ana kuti boma litichitira chitani kuiwala kuti boma ndi anthu ndipo mmodzi mwa anthuwo ndi ine.

Pamene President Lazarus Chakwera akukangalika kuti athandize anthu adziko lonse la Malawi, ntchitoyi sangagwire yekha, akudalira anthu akufuna kwabwino, adindo ndi wina aliyense kuti ndi zochepa zomwe alinazo athandize nzake, ndiye ine ndatengapo gawo langa poyankha pempho lomwe anthu-abale anga akuno adandipempha pa 29 March chakachino pamene ndinabwera kudzacheza pa tchuti cha pasaka.

Choncho lero ndapereka katunduyu ngati yankho ku pempho lawo” watero Ching’ani.

Poyankhulapo, mfumu yayikulu Tsikulamowa yati vuto la njala lomwe ladza kaamba ka kusintha kwa nyengo ndilomwe lakakamiza anthu kuderali kuyamba ulimi wa mthilira ndipo katundu amene a Ching’ani apereka athandiza koposa popititsa patsogolo ulimiwu kuderalo.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular