Mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) Arthur Peter Mutharika lero Lachinayi wagawa chakudya kwa anthu amene akhuzidwa ndi njala ‘mboma la Machinga.
Ku mwambo kunalinso akulu akulu ena a chipanichi monga Bright Msaka, Daudi Chikwanje, Shadric Namalomba ndi ena ambiri.Machinga ndi limodzi mwa maboma omwe akhunzidwa kwambili ndi njala mdziko muno.
Miyezi iwili yapitayi, kunamveka malipoti okuti anthu ena a m’bomali ayamba kudya nyemba za chitedze kamba ka njala.
[…] Source […]