spot_img
Monday, January 6, 2025
spot_img
HomeLatestChakwera akudzudza mizimu ya Malawi osalakwa - Mutharika

Chakwera akudzudza mizimu ya Malawi osalakwa – Mutharika

Mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) Peter Mutharika wati anthu akuvutika m’dziko lino kamba ka utsogoleri wa Chakwera yemwe sakudziwa chomwe akuchita.

Mwachitsanzo, Mutharika wati mafuta akusowa koma Chakwera sakudziwa momwe angathanirane ndi vutoli ndipo ati zinthu zikukwera tsiku ndi tsiku koma a Chakwera alichete kusonyeza kuti sakuganizira anthu omwe anamuika pa mpando.

A Mutharika alonjeza khwimbi la anthu lomwe linali pa bwalo la Thambani m’boma la Mwanza kuti akazalowanso m’boma chaka chamawachi adzaonetsetsa kuti zinthu zofunikira pa moyo wa anthu zizatsike mtengo.

Iye wauzanso anthu aku Mwanza kuti azapaka phula msewu wa Chapanaga-Thambani-Mwanza-Neno-Tsangano.

Kuonjezera apo, ati azamanga Technical College ku Thambani komanso azapitiriza ndondomeko yotsitsa mtengo wamalata ndicholinga choti anthu ambiri m’dziko lino azakhale ndi nyumba zabwino.

Chotero, pulezidenti Mutharika wapempha anthu kuti akalembetse mwa unyinji kalembera wazisankho akayamba mawa pa 28 November 2024 m’bomali ndicholinga choti azachotsetse MCP m’boma.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular