Malingana ndi chikalata chomwe tapeza chikuonetsa kuti nduna ya za migodi a Kenneth Zikhale Ng’oma akufuna Phungu wa mzinda wa Blantyre a Sameer Suleman awapepetse ndi ndalama zokwana 1.5 billion Malawi kwacha.
Malingana ndi chikalatachi chochokera kwa oyimila mulandu a Taulo Attorneys chati phunguyu ayimbidwa mulandu oononga dzina la ndunayi pouza mtundu wa Amalawi nkhani za bodza komanso zopanda pake.
Chikalatachi chati a Suleman mmwezi wa December 2024 adauza mtundu wa Amalawi kuti a Hon Zikhale Ng’oma ndi chigawenga ponena kuti adalemba anthu kuti aphe phunguyu.
A Zikhale akufuna a Suleman afotokozere mtundu wa Amalawi kuti zomwe ankanena ndi zaboza komanso zopanda pake. Phunguyu ampasa maola 24 kuti achite izi akapanda kutero alipira chipepesochi.