Mtsogoleri wa chipani cha DPP, a Peter Mutharika, wati zinthu m’dziko muno zavuta kwambiri pansi pa ulamuliro wa a Lazarus Chakwera.
Mu kuyankhula kwawo madzulo ano kuchokera ku nyumba yawo ku Mangochi, a Mutharika ati ndondomeko yogula zipangizo zotchipa za ulimi ya AIP sikupindula, kusiyana ndi imene inachitika pansi pa ulamuliro wawo ya Fisp, yomwe akuti imakwanitsa kufikira zolinga zomwe adayiyikira.
Iwo ati chipani chawo chikabweleranso m’boma chidzasintha zinthu, poonetsetsa kuti achinyamata amene akusowa ntchito,apeza zochita komanso kuti ndalama zakunja zidzipezeka m’dziko muno kuti anthu ochita malonda adzitha kuchita malonda awo popanda vuto.