Bwalo la Milandu la Resident Magistrate ku Lilongwe lati lidzamva mulandu wa Hannah Jabesi, yemwe amatchuka ndi dzina loti Tamia Ja, pa 20 February chaka chino.
Bwaloli lapereka masiku asanu ndi awiri kumbali yaboma kuti libweretse poyera milandu yomwe oganiziridwayu akuzengedwa.
Oimira Tamia Ja, a Stanley Chirwa, ati ali ndi chiyembekezo kuti pofika tsikuli, mbali yaboma idzakhala yauza oganiziridwayu milandu yomwe wapalamula.
Oimira mbali yaboma, a Mphatso Iphani, ati pakadalipano alibe choti ayankhule.