![](https://www.malawivoice.com/wp-content/uploads/2024/12/Chakwera-budget.jpg)
Powomba mkota pantchito zosiyanasiyana zachitukuko zomwe zachitika m’maboma onse adziko lino pansi pa utsogoleri wawo, Dr Lazarus Chakwera ati aMalawi adzionera okha kuti utsogoleri wawo ndiomangilira dziko lonse monga mtundu umodzi wa aMalawi.
Iwo ati ntchito zamanja awo zikuwachitira umboni ndipo akuyang’ana chitsogolo kuti chitukukochi chipitilire mdziko muno.
Pakadali pano mtsogoleri wadziko linoyu akutuluka m’Nyumba ya Malamulo.
Sipikala wa Nyumba ya Malamulo a Catherine Gotani Hara atseka nyumbayi ndipo aphungu adzakumana Lolemba pa 17 February 2025 kudzapitiriza zokambirana zawo.