![](https://www.malawivoice.com/wp-content/uploads/2025/02/1739602748635.jpg)
Mneneri wa chipani cha MCP, Jessie Kabwira, wati ndizotheka kuti zinthu zina zomwe wayankhula mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera Lachisanu potsekulira nyumba ya malamulo ndi zonama, koma wati boma lawo lachita chitukuko chomwe sichinachitikeposo m’dziko muno.
Izi zili mukilipi yomwe anthu akugawana m’masamba anchezo momwe zikuoneka kuti Kabwira amayankhula ndi anzawo aku chipani cha MCP.
Izi ndi zomwe Kabwira walankhula mukilipiyi:
“Ndanena kale, tikamazimitsa moto sitisankha madzi. it’s possible kuti ma fingers ena might not be correct, so what? Koma taonani zimene tikuona ndimasozi. Nde wina akamakubweretserani kuti koma apapa it’s not correct, let’s talk about zimene mukuona inuyozo.
“Nkhani pano ndiyowonetsa kuti tagwira ntchito. Za accuracy ayi, tikamamenya nkhondo it’s not about it should be 10cm. Ndale it’s not about facts, it’s about perception, nde chonde tisayambire ifeyo wasting time about accuracy here.
“Izi ndi ndale, Chimene tikufuna ndichoti inuyo tulutsani kuti chitukuko chaikidwa in all regions zomwe sizinachitikepo. Sitinaonepo misewu ya quality ngati imene ikuchitikayi, cdf idakwera. Zinazo who cares, we have an election to win colleagues, let’s not split airs here.
“Nde ndikudabwa kuti a good number of our members tikutha nthawi ndikuti pakuti sipali correct, hee mwina a president akunamizidwa. Colleagues we have an enemy panjira, let’s focus on the enemy. It’s DPP that want to finish us, it’s not about semantics, let’s focus, chonde nthawi yatha.”