
Apolisi amanga mayi wina, Comfort Hausi, yemwe anali akuchokera ku ntchito atasinthana naye mawu.
Malingana ndi abale ake, Hausi anapatsidwa mpata kuti adutse pa Chinseu kulowera njira ya paChipiku ndipo wapolisi wina anamuuza kuti afulumire.
Koma malingana ndi Capital FM, wapolisi wina anauza mayiyu kuti achite changu ‘asamangogwedeza matako’ ndipo mayiyu anayankha chipongwe zomwe zinapangitsa kuti apolisiwa amugwire.
Pakadali pano, abale a mayiyu auzidwa kuti adzapite mawa kupolisi kukalondoloza za nkhaniyi.
Apolisi anakalimbanabe ndi anthu ochita zionetsero zodana ndi kukwera mitengo kwa zinthu ndipo utsi okhetsa misozi unakaponyedwabe kufuna kubalalitsa anthu.