spot_img
Monday, March 17, 2025
spot_img
HomeLatestTamanga a Gangata chifukwa chowaganizira kuti amagwilitsa ntchito MSCE imene adayipeza mwachinyengo-Polisi

Tamanga a Gangata chifukwa chowaganizira kuti amagwilitsa ntchito MSCE imene adayipeza mwachinyengo-Polisi

Apolisi amanga wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP mchigawo cha pakati a Alfred Gangata powaganizira mlandu wogwiritsa ntchito setifiketi ya fomu folo imene akuti adaipeza mwachinyengo.

Wofalitsa nkhani za apolisi mdziko muno a Peter Kalaya ati apolisi amanga a Gangata lero iwo atakadzipereka ku likulu la apolisi ku area 30 mu mzinda wa Lilongwe.

A Kalaya ati a Gangata akuganiziridwa kuti setifiketiyi imene adaipeza mchaka cha 2018 pa sukulu ya sekondale ya Chitowo m’boma la Dedza ndi ya chinyengo.

“Zikalata zikusonyeza kuti a Gangata sadakhalepo wophunzira wa sukulu ya sekondale ya Chitowo komanso sadapiteko kukalemba mayeso a fomu folo ku sukuluyi kusonyeza kuti setifiketi imene akugwiritsa ntchito ndi yabodza,” iwo atero.

Iwo ati apolisi akuyembekezereka kupita ndi a Gangata ku bwalo lamilandu masana a lero kapena lachiwiri.

Iwo atsutsa kuti kumangidwa kwa a Gangata ndi kutsatira zifukwa za ndale pomwe dziko lino likukonzekera chisankho cha chaka chino.

“A Gangata apalamula mlandu umene ndi wosemphana ndi gawo 319 la malamulo ozengera milandu. Ife tikamagwira ntchito sitimaona kuti tikugwira ntchito nyengo zake ziti. Sikuti anthu tidziwasiya amene apalamula mlandu powamanga chifukwa tikuyandikira chisankho, timamanga munthu amene waphwanya lamulo nthawi ina iliyonse,” iwo atero.

Wolemba Pemphero Malimba

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular