spot_img
Tuesday, March 18, 2025
spot_img
HomeLatestGOSH!Mighty Wanderers yatchona ku Mozambique, Bus yaonongeka

GOSH!Mighty Wanderers yatchona ku Mozambique, Bus yaonongeka

Timu ya Mighty Wanderers yalephera kufika mdziko muno dzulo kuchokera ku Mozambique komwe imatenga nawo gawo mu Mpikisano wa Songo International Tournament kumapeto a sabata yatha.

Manoma amayenera kufika kuno ku mudzi dzulo koma kamba ka kuonongeka kwa Bus yawo zapangitsa kuti akhalabe ku Mozambique kwa tsiku lina limodzi.

“Ndi zoonadi Bus yathu yaonongeka sikulowa ma gear komano okonza ma galimoto akuionaona kuti mwina ingatheke” anatero mmodzi mwa nthumwi zomwe zili nawo pa ulendowu pouza MLK Sports Desk.

Pakanali pano, Wanderers yaitanitsa Coaster ya hayala yomwe agwiritse ntchito pobwelera kuno Kumudzi potengera kuti sizikudziwika ngati Bus yawo ingatheke kukonza mwa msanga.

Malipoti enaso akuti, osewera omwe akupita ku timu ya dziko lino ya Flames omwe ndi Gaddie Chirwa komaso Wisdom Mpinganjira agwiritsa ntchito Bus ya timu ya Civo Service United pobwelera kuno Kumudzi kuti afike msanga.

Wanderers inamaliza pa nambala ya chiwiri ya Mpikisano wa Songo International Tournament, itagona ku timu ya UD Songo ndi chigoli chimodzi kwa ziii.

Source : Sir Macdonald Luiz Kapalamula

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular