
Aphunzitsi a sukulu za pulaimale omwe adamaliza maphunziro awo pansi pa ndondomeko ya IPTE 13 mpaka 17 ndipo sadalembedwebe ntchito aloza chala boma posalabadira madandaulo awo.
Mtsogoleri wa aphunzitsi-wa Cedric Nyasulu wati iwo akhala akudandaulira boma kuti lisinthe ndondomeko yomwe amagwiritsa ntchito polemba ntchito aphunzitsi-wa ponena kuti imachuluka chinyengo.
Koma iwo ati boma silikuwonetsa chidwi chosintha izi ndipo ati potengera kuti adindo sakumva madandaulo awo iwo sapitilira ndi ganizo lochita ziwonetsero.
Kotero iwo ati ndi aphunzitsi anzakewa adzagwiritsa ntchito bwino lomwe voti yawo mu September muno kuti athandizidwe.