spot_imgspot_img
Thursday, March 20, 2025
spot_img
spot_img
HomeLatestZaka khumi ku ndende pa mlandu okuba K7,000

Zaka khumi ku ndende pa mlandu okuba K7,000

Bwalo la milandu la Lilongwe Resident Magistrate lalamula anyamata awiri onse a zaka 25 kuti akakhale ku ndende zaka khumi kaamba kochitira chipongwe ndikubera munthu 7 sauzande kwacha ndi lamya ya 350 sauzande kwacha.

Malinga ndi wachiwiri kwa mneneli wa polisi ya Lilongwe Constable Khumbo Sanyiwa, awiriwa ndi Victor Chitsinde ndi Embiriyo Kanthiti.

Iwo ati bwaloli linamvetsedwa kuchokera kwa Inspector Bauleni Namasani kuti pa 4 mwezi uno adachitira chipongwe mkulu wina cha pa shop ya Wullian pomwe adamubera katundu osiyanasiyana kuphatikizapo lamya ya Redmi note 11.

Ngakhale adaukana mlanduwu koma mbali ya boma idabweretsa mboni zomwe zidatsimikiza kuti makosanawa adapalamuladi mlanduwu.

Ngakhale adapempha bwalo kuti limumvere chisoni ati poti aka nkoyamba kupalamula, mbali ya boma idati makosanawa adachita zinthu zoopsa komanso kuti sadachita izi mwa ngozi koma kuchita kukonza.

Popereka chigamulo chake, Senior Resident Magistrate Bracious Kondowe adagwirizana ndi mbali ya boma ndipo adalamula kuti awiriwa akakhale ku ndende zaka khumi ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular