
Apolisi m’boma la Chitipa amanga mkulu wina pomuganizira kuti amachita zachisembwere ndi ng’ombe.
Malingana ndi ofalitsankhani za apolisi ku Chitipa, a Gladwell Simwaka, anthu ena adamupezelera mkuluyo, yemwe ndi James Mtambo wazaka 25, usiku wapa 21 akuchita zadamazo ndi ng’ombe.
Mkuluyo akuyembekezeka kuzengedwa mlandu ogona ndi chiweto, zomwe ndizosephana ndi malamulo adziko lino.