
Mtsogoleli wa zokambirana ku nyumba ya malamulo Richard Chimwendo Banda wati chipani chotsutsa cha DPP chikhala mbaliyi kwa 60 zikudzazi.
Chimwendo Banda wati mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera sakuchoka m’boma potengera kuti wapanga chitukuko mosakondera dera lililonse.
Iwo ati boma la DPP linawononga zinthu zambiri m’dziko muno ndipo nkosatheka kuti litengeso boma pa zisankho za chaka chino.
Chimwendo Banda wanena izi mnyumba ya malamulo.