
Wachiwiri kwa Nduna yowona zaubale wa dziko lino ndi maiko ena Patricia Kainga Nangozo wati amakhulupirira kulemekezana pakati pa anthu posatengera maudindo aliwonse.
Malingana ndi a Nangozo ndizomvetsa chisoni komanso zokhumudwitsa kuti Pali malipoti ena abodza womwe akunena kuti Iwo analankhula Mau ena wonyoza phungu wa Dera la kummwera chakummawa mu nzinda wa Blantyre a Sameer Suleman.
Izi zikutsatira kusamvana komwe kunabuka kamba ka malankhulidwe a Suleman womwe akuti anali wosalemekeza ndunayi.
Ndipo pa nthawi yopumira pa zokambiranazi a Kainga anati Iwo anali ndicholinga chokakumana ndi a Suleman pofuna kukambirana nawo mwamtendere pozindikira kuti monga anthu womwe akugwira ntchito yotumikira a Malawi mnyumbayi amayenera kukhala pansi ngati Pali kusamvetsetsana kwa mtundu uli onse.
Koma wachiwiri kwa ndunayi akuti anali wodabwa kwambiri ndi malankhulidwe komanso mawonekedwe awukali a Suleman zomwe anati ndi zinthu zomvetsa chisoni kwambiri polingalira kuti mbali zonse mnyumbayi zimakhala ndi nthawi yochezerana makamaka pomwe akupumulira zokambirana zawo.
Pakadali pano a Kainga atsindika zakufunika kopatsana ulemu pakati pa anthu onse mnyumbayi polingalira maudindo womwe aphungu komanso Nduna za boma Ali nawo pofuna kutukula miyoyo ya anthu mdziko muno.