spot_imgspot_img
Sunday, March 30, 2025
spot_img
spot_img
HomeLatestMwauponda! Sindikuchoka pa mpando- Chakwera

Mwauponda! Sindikuchoka pa mpando- Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wati ngati panali wina adali ndi lingaliro lotenga boma chaka chino ayiwale loto lotere kaamba koti iye sachoka pa mpando.

Iwo ati ali ndi zowayenereza zonse kupambana zisankho zomwe zichitike m’dziko muno m’mwezi wa September.

Dr Chakwera achenjezanso onse omwe ati ali ndi m’chitidwe woba ndalama za boma kuti apeze zina zochita kaamba koti mabowo onse omwe amatululira ndalama zaboma iwo atseka, ngakhale ena akwiya nazo.

Iwo ati pali ena omwe adali m’boma omwe akufuna kubwelera m’boma ndi cholinga chofuna kumapitiriza kuba koma izi sizitheka.

Iwo ayankhula izi potsekulira mkumano wa bungwe la Teveta mu mzinda wa Lilongwe.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular