
Phungu wa nyumba ya malamulo mdera la kumvuma m’boma la Lilongwe wati atolankhani ali ndi kuthekera kwakukulu kozindikilitsa anthu za momwe aphungu akuyendetsera ndalama za mthumba la chitukuko (Community Development Fund – CDF).
A George Zulu ati atolankhani adzikhala ndi kalondolondo wa ndalama mkumabweretsa poyera m’mene ndalamazi zagwilira ntchito m’madera osiyanasiyana.
Iwo anapitiliza kunena kuti anthu sazindikila kuti ndalamayi imayenera kugwira ntchito zanji mchifukwa chake anthu ambiri amaganiza kuti aphungu amangodya ndalamazi.
Popeleka mndandanda wa m’mene iwo agwilitsira ntchito ndalama za thumba la chitukuko mdera lawo phunguyu mwa zina ati akwanitsa kupereka ma school fees kwa ana wokwana 210 ma school osiyanasiyana, komanso kupereka ngongole kwa azimayi ndi achinyamata osiyanasiyana ndi kumanga milatho ndi midadada ya sukulu.
Iwo anatsimikizila atolankhani kuti wofuna kukayendera ndi kulemba zitukuko zawo apite kudelali.
Kenaka a Zulu analangiza atolankhani kuti asamaziyang’anire pansi chifukwa ali ndi ntchito yaikulu mdziko muno pofuna kubweretsa poyera m’mene ndalama za boma zikugwilira ntchito m’magawo osiyanasiyana.