
Mtsogoleli wa zipani zotsutsa mnyumba ya malamulo Dr. George Chaponda wati kulowa m’boma kwa chipani cha MCP ndi ngozi yomwe simayenera kuchitika.
Chaponda wati chipani cha Democratic Progressive (DPP) chidzapambana chisankho cha pa 16 September chaka chino.
Dr. Chaponda anena izi m’mawa uno pomwe aphungu a nyumba yamalamulo akukumana kotsiliza chiwasankhireni pachisankho cha 2019.
Iwo akuti a Peter Mutharika ndi omwe angathane ndi mavuto omwe dziko lino likukumana nawo.
Wolemba: Esther Nyirongo, Lilongwe.