spot_img
Thursday, December 12, 2024
spot_img
HomeLatestFND YAPEMPHA BOMA KUYIMITSA LAMULO LA ZANKHALANGO MPAKA LITAYIKA NDONDOMEKO ZOTHANDIZIRA ANTHU...

FND YAPEMPHA BOMA KUYIMITSA LAMULO LA ZANKHALANGO MPAKA LITAYIKA NDONDOMEKO ZOTHANDIZIRA ANTHU OSAUKA

Lamulo lomwe boma la Malawi lakhazikitsa pankhani zokhudza zankhalango, lingathe kukhala lamulo lophinja komanso kunzunza amalawi osauka ambiri ngati boma siliika ndondomeko ndi njira zina zimene amalawi osauka angathe kugwiritsa ntchito.  

Lamulori mmene lilili panopa, likuoneka kuti anthu olemera akonza lamulo lonzunza anthu osauka kuti olemelawo ankhale ndi mwai wa malonda amakala ndi zina zopezeka munkhalango. Ndipo ngati boma litapitilire ndi ganizoli, anthu osauka avutika kwambiri komanso, kupitilira kukhala osauka.  

Angakhale kuti cholinga cha lamulori ndi kuteteza chilengedwe, mitengo kudzanso nkhalango za mdziko lino kudzera kunthetsa mchitidwe odula mitengo ndi kuotcha makala omwe waononga chilengedwe cha mdziko la Malawi, tikuona kuti lamuloli labwera munthawi yolakwika zedi chifukwa chakuti amalawi ambiri afinyika ndi nkhani za chuma.

Komanso pakadali pano, dziko la Malawi silinakhazikitse ndondomeko zabwino zimene zingathe kufikira amalawi onse pa nkhani ya mphavu zogwiritsa ntchito pophika ndi zina zotero.   Amalawi ochepa zedi, ochepera 10 mwa anthu 100 alionse, omwe ali ndikuthekera kogwiritsa mphamvu zamagetsi mdziko lino.

Komanso, kwa amalawi ochepawo, magetsi akenso akumakhala osakwanira ndipo akumangozimazima. Amalawi ambiri omwe akufuna magetsi sakutha kupatsidwa ndi bungwe lija la ESCOM ndipo anthu ambiri akhala kuposa zaka ziwiri kuti magetsi awo alumikizidwe.  

Anthu akhanikhani ku Malawi, anthu oposera 97 mwa anthu 100 alionse, amadalira nkhuni kapena makala. Chodandaulitsa, zinthu ziwiri zimenezi ndi zimene lamulo latsopanoli likufuna kuthetsa. Chodetsa nkhawa ndi chakuti angakhale makala amene akunenedwa kuti ali bwino kuchilengedwe ndi okwera mtengo kwambiri pamene nthumba la 10kg likumagulitsidwa pamtengo woposera K6,000, kudzanso apo amapezeka mmalo ochepa mdziko lino.  

Mukaunikira zinthu zonsezi, chinthu chimene chingathe kukhala mlowa mmalo wa makala kudzanso nkhuni mwina chingathe kukhala mphamvu za gas. Komano kuti gas akhale mphamvu yodalilika, pakufunika kuti pakhazikitsidwe ndondomeko komanso ziganizo kuchokera ku boma zothandiza amalawi.   Pakadali pano, mtengo wa gas ndiokwera kwambiri ndipo amalawi ambiri omwe ali osauka sangathe kukwanitsa kugwiritsa ntchito. Mtengo wa gas pakanali pano uli pa K2,956 per kg ndipo mabanja ambiri amafunika kugwiritsa gas osachepera14kg pamwezi.

Izi zikutathauza kuti pamwezi, banja likuyenera kugula gas osachepera ndalama zokwana K41,384 pa mwezi, zimene zili zinthu zosatheka kwa amalawi ambiri. Mtengo wa mbaula yaying’ono ya gas ikudutsa pamtengo wa K95,000 imodzi ndipo ndi mtengo wokwera kwambiri kwa amalawi ochuluka zedi.   Ndi mitengo imeneyi ya gas kudzanso mbaula zake, ndikuwalakwira kwambiri amalawi kumayembekezera kuti angathe kugwiritsa ntchito moto wa gas mmalo mwa nkhuni ndi makala.

Ndichifukwa chake ife a FND tikupempha bola la Malawi litayamba layimitsa ganizo la lamulori kwa zaka ziwiri.    Muzaka ziwiri zomwe tikupempha kuti lamulo liyimitsidwe, boma la Malawi likonze ndondomeko zomwe zingathe kuthandiza amalawi ambiri kukwanitsa kugwiritsa ntchito moto wa gas. Tikupempha boma kuchitapo zinthu izi mwa zina zambiri;

  1. Kuyika ndondomeko zothandiza anthu osauka kupeza nawo mwayi ogula mbaula za gas pamtengo osaposela K10,000 kudzera munjira ya sabuside. Anthu osauka omwe anganthandizidwe ndindondomekoyi angathe kuwapeza pounika anthu omwe akhala akupindula mundondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo (AIP) kudzanso amene amapindula ndi ndondomeko ya mtukula pa nkhomo.

 2. Kuchotsa misokho yomwe anthu amalipira poyitanitsa zipangizo zophikira za gas monga ma cooker, ma stove, mbaula zing’onozing’ono, kudzanso ma gas cylinders.

3. Kuyika ndondomeko yokuti anthu osauka azintha kugula gas pamtengo wotchipa wosaposera K1,500/kg kudzera munjira ya sabuside.

4. Kukhazikitsa njira zophunzitsira amalawi ubwino ndi kagwiritsidwe ka gas. Kuno kwanthu ku Malawi, kuli kusamvetsetsa pa nkhani yakagwiritsidwe ka gas.

5. Boma liwonetsetse kuti magetsi akupezeka ndipo bungwe la ESCOM likwanitse kulumikiza anthu omwe akhala akudikira magetsi kuposera miyezi isanu ndi umodzi kupita mtsogolo.

Ife a FND, tikupempha boma kupanga chiganizo pankhani yoyimitsa ndondomeko ya lamuloli monga umo tapemphera kwa zaka ziwiri. Panthawi imeneyi boma liyike ndondomeko zoteteza anthu osauka kuti asavutike kamba ka lamulo la zankhalangoli. Lamuloli lisakhale chipsinjo kwa anthu osauka. 

Ngati boma silikwanilitsa kuunika komanso kuchitapo kanthu pazinthu takambazi, ife a FND tidzamemeza anthu osauka omwe apsinjidwe, komanso kuzunzika ndi lamuloli, kukana ndi kutsutsa lamuloli.

Signed    

Fryson Chodzi                                                              Bright Kampaundi

NATIONAL COORDINATOR                                              CHAIRPERSON

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular