Nthumwi ku msonkhano wa komiti yaikulu ya chipani cha DPP zagwirizana kuti msonkhano wa ukulu osankha adindo achipanichi uchitika ku NRC ku Lilongwe pa 15 mpaka pa 16 December chaka chino.
Komitiyi i yasankhanso a Nicholas Dausi ngati wapampando wa komiti yoyendetsa msonkhano wa komvenshoniyo ndipo wachiwiri wawo, a Baxter Kita.
Komiti-yi yasankhanso a Kondwani Ng’ong’ola ngati oyang’anira za chakudya ndi malo ogona ndipo achiwiri awo, a Joseph Mavuto Kachali
Samuel Phillimon ndi a Ralph Jooma asankhidwa kukhala akulu akulu owona zamayendedwe pa msonkhano wa ukulu wu.
Mlembi wa mkulu wa chipanichi a Grezelder Jeffrey awasankha kukhala owona za anthu obwera ku msonkhanowu.