spot_img
Saturday, December 28, 2024
spot_img
HomeLatestNdine munthu opereka osati ‘masikini’ ongopemphesa – Norman Chisale 

Ndine munthu opereka osati ‘masikini’ ongopemphesa – Norman Chisale 

Yemwe akupikitsana nawo ngati mkulu woyang’anira achinyamata m’chipani cha Democratic Progressive – DPP, a Norman Chisale, ati iwo azakhala mtsogoleri opereka osati ongopemphesa kwa anthu ngati momwe ena amachitira.   

A Chisale, omwe amadziwika bwino ndi dzina loti “Msamaliya Wa Chufundo” kaamba ka mtima wawo opereka kwa anthu osowa, ati pambali pa kupereka iwo azawonetsetsa kuti achinyamata ku Chipani cha DPP sakudyeredwa masuku pa mutu.

“Ndizakhala munthu odziwa ntchito yake, osadya ndalama za achinyamata, osapempha mafuta koma kupereka mafuta kwa achinyamata,” atero a Chisale, omwenso ndi wachitetezo wa mtsogoleri wakale wa dziko lino, a Peter Mutharika. 

M’mbuyomu, anthu ena ochokera m’boma la Ntcheu komwe ndi kwawo kwa a Chisale anawapempha iwo kuti aziyimilire ngati phungu wa nyumba ya malamulo pa chisankho chomu m’chaka cha 2025, ponena kuti ali ndi mphatso ya utsogoleri, a chifundo komanso chikondi Kwa anthu.

Chipani cha DPP chichititsa msokhano wake wa ukulu pa 26 komanso 27 December chaka chino, komwe nthumwi zikasankhe adindo atsopano, omwe kuphatizipo mkulu owona za achinyamata komanso mtsogoleri wa chipanichi.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular