spot_img
Wednesday, January 15, 2025
spot_img
HomeLatestChamba kuno ayi, Watero Chakwera

Chamba kuno ayi, Watero Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wakana kuvomereza bilo yokhudza kuvomereza chamba cha m’dziko muno ngati mbali imodzi ya chamba chovomelezedwa kulimidwa ngati pali chiphanso,Canabis Regulatory Amendment kukhala lamulo.

Kudzera mkalata yomwe nyumba ya boma yatulutsa, mtsogoleriyu sanasayinire lamuloli kaamba koti magulu ena anthu okhudzidwa akhala akupeleka maganizo osephana pa za zotsatira zovomeleza lamuloli.

Pakadali pano a Chakwera ati pakufunika ndondomeko yofuna kumva maganizo a nzika komanso kuzindikilitsa a Malawi zomwe lamuloli likufotokoza.

Kupatula kusatsindikiza lamulo la Chambali, Mtsogoleri wa dziko lunoyu wasayinira lamulo lokhudza achikulire, lamulo lokhudza nthambi za mphamvu za magetsi komanso ma bilo ena omwe boma la Malawi likubweleka ndalama zomwe zithandizire kubweletsa chitukuko cha madzi kuchokera ku nyanja ya Malawi.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular