spot_img
Monday, December 16, 2024
spot_img
HomeLatest"Kaya wina afune asafune DPP itenganso boma"

“Kaya wina afune asafune DPP itenganso boma”

Chipani cha Democratic Progressive (DPP) chati chili ndi chiyembekezo chodzatenganso boma pa chisankho chapatatu chomwe chikubwera chaka chamawa.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi m’chigawo chakum’mawa Bright Msaka wanena izi pa msonkhano wa ndale womwe unachitikira ku wadi ya Mwasa m’boma la Mangochi.

Msaka adati boma lomwe lilipoli lalephera ndipo adanenetsa kuti DPP ndi chipani chokhacho chomwe chimasamala za umoyo wa anthu.

Iye walimbikitsa anthu kidelari kuti avotere khansala wa DPP, Kida Adam, ngati njira imodzi yobweretsa chipani cha DPP m’boma.

M’mawu ake, gavanala wa chipanichi m’chigawo cha kum’mawa a Imran Mtenje wapempha anthu aku wadi ya Mwasa kuti adzatsatire malamulo ndi ndondomeko zonse zomwe bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission lidakhazikitsa pa nthawi ya chisankhochi pomwe kuponya voti kuchitike lachiwiri likudzali.

Bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) likuchititsa zisankho zapadera za makhansala mu wadi ya Mwasa ku Mangochi ndi Chilaweni ku Blantyre.- CAPITAL FM

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular